Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 30:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Taonani, dzina la Yehova licokera kutari, mkwiyo wace uyaka, malawi ace ndi akuru; milomo yace iri yodzala ndi ukali, ndi lilime lace liri ngati moto wonyambita;

28. ndi mpweya wace uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi copetera ca cionongeko; ndi capakamwa calakwitsa, cidzakhala m'nsagwada za anthu.

29. Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi citoliro, kufikira ku phiri la Yehova, ku thanthwe la Israyeli,

30. Ndipo Yehova adzamveketsa mau ace a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lace, ndi mkwiyo wace waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.

31. Pakuti ndi mau a Yehova Asuri adzatyokatyoka, ndi ndodo yace adzammenya.

32. Ndipo nthawi zonse Yehova adze vakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyana-thunyana, Iye adzamenyana nao.

33. Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde cifukwa ca mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wacewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wasulfure.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 30