Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 28:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati cimphepo ca matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.

3. Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu adzaponderezedwa;

4. ndi duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu pa cigwa ca nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kuca malimwe asanafike; polona wakupenya imeneyo, amaidya iri m'dzanja lace.

5. Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ace otsala:

6. ndipo adzakhala mzimu wa ciweruziro kwa oweruza mirandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pacipata.

7. Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi cakumwa caukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza.

8. Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udio, palibe malo okonzeka.

9. Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere?

10. Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.

11. Iai, koma ndi anthu a milomo yacilendo, ndi a lilume lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;

12. amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.

13. Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.

14. Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 28