Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 28:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;

16. cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.

17. Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.

18. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kubvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalepereka; popita mliri woopsya udzakuponderezani pansi.

19. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; cifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsya kokha, kumva mbiri yace.

20. Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi copfunda cacepa, sicingamfikire.

21. Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'cigwa ca Gibeoni; kuti agwire nchito yace, nchito yace yacilendo, ndi kuti acite cocita cace, cocita cace cacilendo.

22. Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za cionongeko cotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.

23. Cherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.

24. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? kodi amacocolabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?

25. Atakonza tyatyatya pamwamba pace, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza citowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ace osankhika, ndi mcewere m'maliremo?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 28