Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 28:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu.

15. Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;

16. cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.

17. Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.

18. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kubvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalepereka; popita mliri woopsya udzakuponderezani pansi.

19. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; cifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsya kokha, kumva mbiri yace.

20. Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi copfunda cacepa, sicingamfikire.

21. Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'cigwa ca Gibeoni; kuti agwire nchito yace, nchito yace yacilendo, ndi kuti acite cocita cace, cocita cace cacilendo.

22. Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za cionongeko cotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.

23. Cherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.

24. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? kodi amacocolabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 28