Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 27:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndiribe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? ndiziponde ndizitenthe pamodzi.

5. Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nacite nane mtendere; inde, acite nane mtendere.

6. M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israyeli adzaphuka ndi kucita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi.

7. Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?

8. Munalimbana naye pang'ono, pamene munamcotsa; wamcotsa iye kuomba kwace kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.

9. Cifukwa cace, mwa ici coipa ca Yakobo cidzafafanizidwa, ndipo ici ndi cipatso conse cakucotsa cimo lace; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.

10. Pakuti mudzi wocingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati cipululu; mwana wa ng'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamariza nthambi zace.

11. Ponyala nthambi zace zidzatyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; cifukwa cace Iye amene anawalenga sadzawacitira cisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.

12. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wace, kucokera madzi a nyanja, kufikira ku mtsinje wa Aigupto, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israyeli.

13. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikuru lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asuri, ndi opitikitsidwa a m'dziko la Aigupto; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 27