Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 25:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, cifukwa mwacita zinthu zodabwitsa, ngakhale: zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

2. Cifukwa Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse.

3. Cifukwa cace anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mudzi wa mitundu yakuopsya udzakuopani Inu.

4. Cifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kubvutidwa kwace, pobisalira cimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsya kufanana ndi cimphepo cakuomba chemba.

5. Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsya idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa.

6. Ndipo m'phiri limendi Yehova wa makamu adzakonzera anthu ace onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 25