14. Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; pakuti linga lanu lapasulidwa.
15. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Turo adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, cidzakhala kwa Turo monga m'nyimbo ya mkazi wadama.
16. Tenga mngoli, yendayenda m'mudzi, iwe mkazi wadama, amene unaiwalika; yimba zokoma, curukitsa nyimbo, kuti ukumbukiridwe.
17. Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Turo, ndipo iye adzabwerera ku mphotho yace, nadzacita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.