Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 23:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pita pakati pa dziko lako monga Nile, iwe mwana wamkazi wa Tarisi; palibenso lamba.

11. Iye watambasula dzanja lace panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira za amalonda, kupasula malinga ace.

12. Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wobvutidwa, mwanawamkazi wa Zidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.

13. Taonani, dziko la Akasidi; anthu awa sakhalanso; Asuri analiika ilo likhale la iwo okhala m'cipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ace; nalipasula.

14. Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; pakuti linga lanu lapasulidwa.

15. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Turo adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, cidzakhala kwa Turo monga m'nyimbo ya mkazi wadama.

16. Tenga mngoli, yendayenda m'mudzi, iwe mkazi wadama, amene unaiwalika; yimba zokoma, curukitsa nyimbo, kuti ukumbukiridwe.

17. Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Turo, ndipo iye adzabwerera ku mphotho yace, nadzacita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.

18. Malonda ace ndi mphotho yace zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; cifukwa malonda ace adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, nabvale caulemu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 23