Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 23:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Turo.Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; cifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kucokera ku dziko la Kitimo kwabvumbulutsidwa kwa iwo.

2. Khalani cete, inu okhala m'cisumbu; iwe amene anakudzazanso amalonda a ku Zidoni, opita m'nyanja.

3. Ndi pa nyanja zazikuru anapindula ndi mbeu za ku Sihori ndizo dzinthu za ku Nile; ndi kumeneko kunali msika wa amitundu.

4. Khala ndi manyazi, iwe Zidoni; cifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.

5. Pofika mbiriyo ku Aigupto, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Turo.

6. Olokani inu, kunka ku Tarisi, kuwani, inu okhala m'cisumbu.

7. Kodi umene ndi mudzi wanu wokondwa, wacikhalire kale lomwe, umene mapazi ace anaunyamula kunka nao kutari kukhalako?

8. Ndani wapanga uphungu uno pa Turo, mudzi umene upereka akorona, amalonda ace ali akalonga, ogulitsa ace ali olemekezeka pa dziko lapansi?

9. Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.

10. Pita pakati pa dziko lako monga Nile, iwe mwana wamkazi wa Tarisi; palibenso lamba.

11. Iye watambasula dzanja lace panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira za amalonda, kupasula malinga ace.

12. Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wobvutidwa, mwanawamkazi wa Zidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.

13. Taonani, dziko la Akasidi; anthu awa sakhalanso; Asuri analiika ilo likhale la iwo okhala m'cipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ace; nalipasula.

14. Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; pakuti linga lanu lapasulidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 23