Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 20:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda marisece ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale cizindikilo ndi codabwitsa kwa Aigupto ndi kwa Etiopia;

4. momwemo mfumu ya Asuri idzatsogolera kwina am'nsinga a Aigupto, ndi opitikitsidwa a Etiopia, ana ndi okalamba, amarisece ndi opanda nsapato, ndi matako osabvala, kuti acititse manyazi Aigupto.

5. Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, cifukwa ca Kusi, amene anawatama, ndi Aigupto, amene anawanyadira.

6. Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asuri, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 20