Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 14:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti Ambuye adzamcitira cifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israyeli, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo acilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza ku nyumba ya Yakobo.

2. Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa ku malo a kwao; ndipo a nyumba ya Israyeli adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisrayeli adzalamulira owabvuta.

3. Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa cisoni cako, ndi nsautso yako, ndi nchito yako yobvuta, imene anakugwiritsa,

4. pamenepo udzayimbira mfumu ya ku Babulo nyimbo iyi yancinci, ndi kuti, Wobvuta wathadi! mudzi wagolidi wathadi!

5. Yehova watyola mkunkhu wa woipa, ndodo yacifumu ya wolamulira.

6. Wokantha anthu mwaukali kuwakantha cikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.

7. Dziko lonse lapuma, liri du; iwo ayamba kuyimba nyimbo,

8. Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebano, ndi kunena, Cigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.

9. Kunsi kwa manda kugwedezeka, cifukwa ca iwe, kukucingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuru akuru a dziko lapansi; kukweza kucokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.

10. Onse adzabvomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? kodi iwe wafanana nafe?

11. Cifumu cako catsitsidwa kunsi ku manda, ndi phokoso la mingoli yako; mbozi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.

12. Wagwadi kucokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbanda kuca! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!

13. Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;

14. ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.

15. Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje.

16. Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 14