Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 8:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?

10. Cifukwa cace ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita zonyenga.

11. Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.

12. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita zonyansa? iai, sanakhala ndi manyazi, sananyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.

13. Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawacokera.

14. Tikhaliranji ife? tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale cete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife cete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamcimwira Yehova.

15. Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

16. Kumina kwa akavalo ace kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo acewo olimba; cifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo.

17. Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.

18. Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa cisoni cace! mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.

19. Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ocokera ku dziko lakutari: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe Mfumu yace? Cifukwa canji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zacabe zacilendo?

20. Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 8