Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 8:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Tikhaliranji ife? tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale cete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife cete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamcimwira Yehova.

15. Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

16. Kumina kwa akavalo ace kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo acewo olimba; cifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo.

17. Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.

18. Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa cisoni cace! mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.

19. Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ocokera ku dziko lakutari: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe Mfumu yace? Cifukwa canji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zacabe zacilendo?

20. Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.

21. Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.

22. Kodi mulibe bvunguti m'Gileadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kucira mwana wamkazi wa anthu anga?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 8