Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 8:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzaturutsa m'manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akuru ace, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m'Yerusalemu,

2. ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.

3. Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m'malo monse m'mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu.

4. Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzacoka, osabweranso?

5. Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu cibwererere? agwiritsa cinyengo, akana kubwera.

6. Ndinachera khutu, ndinamva koma sananena bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zace, ndi kuti, Ndacita ciani? yense anatembenukira njira yace, monga akavalo athamangira m'nkhondo.

7. Inde, cumba ca mlengalenga cidziwa nyengo zace; ndipo njiwa ndi namzeze ndi cingaru ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa ciweruziro ca Yehova.

8. Bwanji muti, Tiri ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lacita zonyenga,

9. Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?

10. Cifukwa cace ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita zonyenga.

11. Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.

12. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita zonyansa? iai, sanakhala ndi manyazi, sananyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 8