Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 51:20-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Iwe ndiwe cibonga canga ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzatyolatyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21. ndi iwe ndidzatyolatyola kavalo ndi wakwera wace;

22. ndi iwe ndidzatyolatyola gareta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzatyolatyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzatyolatyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzatyolatyola mnyamata ndi namwali;

23. ndi iwe ndidzatyolatyola mbusa ndi zoweta zace; ndi iwe ndidzatyolatyola wakulima ndi gori la ng'ombe lace; ndi iwe ndidzatyolatyola akazembe ndi ziwanga,

24. Ndipo ndidzabwezera Babulo ndi okhala m'Kasidi zoipa zao zonse anazicita m'Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.

25. Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.

26. Ndipo sadzacotsa pa iwe mwala wa pangondya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

27. Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenaza; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati mandowa.

28. Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ace, ndi ziwanga zace zonse, ndi dziko lonse la ufumu wace.

29. Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babulo ziripobe, zoti ayese dziko la Babulo bwinja lopanda wokhalamo.

30. Olimba a ku Babulo akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zace zapsya ndi moto; akapici ace atyoka.

31. Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzace, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzace, kukauza mfumu ya ku Babulo kuti mudzi wace wagwidwa ponsepo;

32. pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.

33. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwana wamkazi wa Babulo akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.

34. Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwace ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine,

35. Wokhala m'Ziyoni adzati, Ciwawa anandicitira ine ndi thupi langa cikhale pa Babulo; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi.

36. Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera cilango cifukwa ca iwe; ndidzaphwetsa nyanja yace, ndidzaphwetsa citsime cace.

37. Ndipo Babulo adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, cizizwitso, cotsonyetsa, wopanda okhalamo.

38. Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzacita nthulu ngati ana a mikango.

39. Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone cigonere, asanyamuke, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 51