Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 51:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.

12. Muwakwezere mbendera makoma a Babulo, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kucita comwe ananena za okhala m'Babulo.

13. Iwe wokhala pa madzi ambiri, wocuruka cuma, cimariziro cako cafika, cilekezero ca kusirira kwako.

14. Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mpfuu.

15. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yace, ndi luso anayala thambo;

16. pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.

17. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golidi acitidwa manyazi ndi fanizo lace losema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya m'menemo.

18. Ngwacabe, ciphamaso; nthawi yakulangidwa kwao adzatayika.

19. Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndi mtundu wa colowa cace, dzina lace ndi Yehova wa makamu.

20. Iwe ndiwe cibonga canga ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzatyolatyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21. ndi iwe ndidzatyolatyola kavalo ndi wakwera wace;

22. ndi iwe ndidzatyolatyola gareta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzatyolatyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzatyolatyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzatyolatyola mnyamata ndi namwali;

23. ndi iwe ndidzatyolatyola mbusa ndi zoweta zace; ndi iwe ndidzatyolatyola wakulima ndi gori la ng'ombe lace; ndi iwe ndidzatyolatyola akazembe ndi ziwanga,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 51