Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:7-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitiparamula mlandu, cifukwa iwo anacimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, ciyembekezo ca atate ao.

8. Thawani pakati pa Babulo, turukani m'dziko la Akasidi, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.

9. Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babulo msonkhano wa mitundu yaikuru kucokera ku dziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babulo adzacotsedwa; mibvi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera cabe.

10. Ndipo Kasidi adzakhala cofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova.

11. Cifukwa mukondwa, cifukwa musekerera, inu amene mulanda colowa canga, cifukwa muli onenepa monga ng'ombe yamsoti yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;

12. amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, cipululu, dziko louma, bwinja.

13. Cifukwa ca mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babulo adzadabwa, adzatsonyera pa zobvuta zace zonse.

14. Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.

15. Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.

16. Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.

17. Israyeli ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampitikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asuri; ndipo pomariza Nebukadirezara uyo watyola mafupa ace.

18. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babulo ndi dziko lace, monga ndinalanga mfumu ya Asuri.

19. Ndipo ndidzabwezeranso Israyeli ku busa lace, ndipo adzadya pa Karimeli ndi pa Basana, moyo wace nudzakhuta pa mapiri a Efraimu ndi m'Gileadi.

20. Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israyeli zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zocimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati cotsala.

21. Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala m'Pekoli, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, cita monga mwa zonse ndinakuuza iwe.

22. Phokoso la nkhondo liri m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukuru.

23. Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kutyoka! Babulo wasandulca bwinja pakati pa amitundu!

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50