Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zirikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'cipangano ca muyaya cimene sicidzaiwalika.

6. Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; acoka kuphiri kunka kucitunda; aiwala malo ao akupuma.

7. Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitiparamula mlandu, cifukwa iwo anacimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, ciyembekezo ca atate ao.

8. Thawani pakati pa Babulo, turukani m'dziko la Akasidi, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.

9. Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babulo msonkhano wa mitundu yaikuru kucokera ku dziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babulo adzacotsedwa; mibvi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera cabe.

10. Ndipo Kasidi adzakhala cofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova.

11. Cifukwa mukondwa, cifukwa musekerera, inu amene mulanda colowa canga, cifukwa muli onenepa monga ng'ombe yamsoti yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;

12. amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, cipululu, dziko louma, bwinja.

13. Cifukwa ca mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babulo adzadabwa, adzatsonyera pa zobvuta zace zonse.

14. Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.

15. Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.

16. Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50