Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:19-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ndidzabwezeranso Israyeli ku busa lace, ndipo adzadya pa Karimeli ndi pa Basana, moyo wace nudzakhuta pa mapiri a Efraimu ndi m'Gileadi.

20. Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israyeli zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zocimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati cotsala.

21. Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala m'Pekoli, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, cita monga mwa zonse ndinakuuza iwe.

22. Phokoso la nkhondo liri m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukuru.

23. Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kutyoka! Babulo wasandulca bwinja pakati pa amitundu!

24. Ndakuchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babulo, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, cifukwa walimbana ndi Yehova.

25. Yehova watsegula pa nyumba ya zida zace, ndipo waturutsa zida za mkwiyo wace; pakuti Ambuye Yehova wa makamu, ali ndi nchito m'dziko la Akasidi.

26. Tadzani kudzamenyana ndi iye kucokera ku malekezero ace, tsegulani pa nkhokwe zace; unjikani zace monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.

27. Iphani ng'ombe zamphongo zace zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.

28. Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babulo, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera cilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.

29. Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.

30. Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndi anthu ankhondo ace onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.

31. Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.

32. Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.

33. Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.

34. Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50