Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene ananena Yehova za Babulo, za dziko la Akasidi, mwa Yeremiya mneneri.

2. Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babulo wagwidwa, Beli wacitidwa manyazi, Merodake watyokatyoka, zosema zace zacitidwa manyazi, mafano ace atyokatyoka.

3. Pakuti mtundu wa anthu udzaturuka kumpoto kudzamenyana naye, udzacititsa dziko lace bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.

4. Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israyeliadzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao.

5. Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zirikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'cipangano ca muyaya cimene sicidzaiwalika.

6. Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; acoka kuphiri kunka kucitunda; aiwala malo ao akupuma.

7. Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitiparamula mlandu, cifukwa iwo anacimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, ciyembekezo ca atate ao.

8. Thawani pakati pa Babulo, turukani m'dziko la Akasidi, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.

9. Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babulo msonkhano wa mitundu yaikuru kucokera ku dziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babulo adzacotsedwa; mibvi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera cabe.

10. Ndipo Kasidi adzakhala cofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50