Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 49:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israyeli alibe ana amuna? alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi cifukwa canji, ndi anthu ace akhala m'midzi mwace?

2. Cifukwa cace, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mpfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ace akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israyeli adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

3. Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, mubvale ciguduli; citani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.

4. Cifukwa canji udzitamandira ndi zigwa, cigwa cako coyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira cuma cace, nati, Adza kwa ine ndani?

5. Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akucokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ace, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osocera.

6. Koma pambuyo pace ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 49