Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 48:31-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Cifukwa cace ndidzakuwira Moabu; inde, ndidzapfuulira Moabu yense, adzalirira anthu a ku Kirere.

32. Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.

33. Ndipo kusekera ndi kukondwa kwacotsedwa, ku munda wobala ndi ku dziko la Moabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kupfuula; kupfuula sikudzakhala kupfuula.

34. Kuyambira kupfuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zoari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.

35. Ndiponso ndidzaletsa m'Moabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yace.

36. Cifukwa cace mtima wanga umlima Moabu monga zitolilo, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kireresi monga zitolilo, cifukwa cace zakucuruka zace adadzionera zatayika.

37. Pakuti mitu yonse iri yadazi, ndipo ndebvu ziri zosengedwa; pa manja onse pali pocekedwa-cekedwa, ndi pacuuno ciguduli.

38. Pamwamba pa macindwi a Moabu ndi m'miseu mwace muli kulira monse monse; pakuti ndaswa Moabu monga mbiya m'mene mulibe cikondwero, ati Yehova.

39. Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Moabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Comweco Moabu adzakhala coseketsa ndi coopsera onse omzungulira iye.

40. Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati ciombankhanga, adzamtambasulira Moabu mapiko ace.

41. Keroti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Moabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42. Ndipo Moabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, cifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 48