Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.