Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 46:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.

9. Kwerani, inu akavalo; citani misala, inu magareta, aturuke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira cikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.

10. Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.

11. Kwera ku Gileadi, tenga bvunguti, namwali iwe mwana wa Aigupto; wacurukitsa mankhwala cabe; palibe kucira kwako.

12. Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kupfuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.

13. Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo adzafika adzakantha dziko la Aigupto.

14. Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 46