Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 46:25-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Aigupto, pamodzi ndi milungu yace, ndi mafumu ace; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;

26. ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'manja a atumiki ace; pambuyo pace adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.

27. Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usacite mantha, iwe Israyeli: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kucokera kutari, ndi mbeu yako ku dziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye,

28. Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndiri ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi ciweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 46