Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 43:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse: a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera ku mitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;

6. ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao Wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, mwana wace wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wace wa Neriya;

7. ndipo anadza nalowa m'dziko la Aigupto; pakuti sanamvera mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

8. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti,

9. Tenga miyala yaikuru m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;

10. ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wace wacifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaibvundikira ndi hema wacifumu wace.

11. Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Aigupto; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.

12. Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Aigupto; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzipfunda ndi dziko la Aigupto, monga mbusa abvala cobvala cace; nadzaturuka m'menemo ndi mtendere.

13. Ndipo adzatyola mizati ya zoimiritsa za kacisi wa dzuwa, ali m'dziko la Aigupto; ndi nyumba za milungu ya Aigupto adzazitentha ndi moto.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 43