Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 43:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

2. pamenepo ananena Azariya mwana wace wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumiza iwe kudzanena, Musalowe m'Aigupto kukhala m'menemo;

3. koma Baruki mwana wace wa Neriya aticicizira inu, mutipereke m'dzanja la Akasidi, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babulo.

4. Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvera mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.

5. Koma Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse: a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera ku mitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;

6. ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao Wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, mwana wace wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wace wa Neriya;

7. ndipo anadza nalowa m'dziko la Aigupto; pakuti sanamvera mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

8. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti,

9. Tenga miyala yaikuru m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;

10. ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wace wacifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaibvundikira ndi hema wacifumu wace.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 43