Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 40:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.

13. Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,

14. nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismayeli mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvera iwo.

15. Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismayeli mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; cifukwa canji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?

16. Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usacite ici; pakuti unamizira Ismayeli.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 40