Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismayeli mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; cifukwa canji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?