Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 40:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babulo.

2. Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera coipa ici malo ano;

3. ndipo Yehova wacitengera, ndi kucita monga ananena, cifukwa mwacimwira Yehova, ndi kusamvera mau ace, cifukwa cace cinthu ici cakufikirani.

4. Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babulo, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babulo, tsala; taona, dziko lonse liri pamaso pako; kuli konse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 40