Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 39:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.

11. Ndipo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,

12. Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umcitire monga iye adzanena nawe.

13. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkuru wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Nerigalisarezari mkuru wa alauli, ndi akuru onse a mfumu ya ku Babulo;

14. iwonso anatumiza, namcotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.

15. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m'bwalo la kaidi, kuti,

16. Pita, ukanene kwa Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osaucitira zabwino; ndipo adzacitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 39