Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mudzi, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babulo.