Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 39:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cacisanu ndi cinai ca Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ndi nkhondo yace yonse, ndi kuumangira misasa.

2. Caka cakhumi ndi cimodzi ca Zedekiya, mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai, mudzi unabooledwa.

3. Ndipo akuru onse a mfumu ya ku Babulo analowa, nakhala m'cipata capakati, Nerigalisarezara, Samgari Nebo, Sarisekimu, mkuru wa adindo, Nerigalisarezara mkuru wa alauli ndi akuru ena onse a mfumu ya ku Babulo.

4. Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa naturuka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa cipata ca pakati pa makoma awiri; ndipo iye anaturukira pa njira ya kucidikha.

5. Koma nkhondo ya Akasidi inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.

6. Pamenepo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya ku Ribila pamaso pace; mfumu ya ku Babulo niphanso aufulu onse a Yuda.

7. Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m'zigologolo, kunka naye ku Babulo.

8. Ndipo Akasidi anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.

9. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mudzi, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babulo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 39