Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 38:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, comweco kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.

21. Koma ngati mukana kuturuka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:

22. Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzaturutsidwa kunka kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.

23. Ndipo adzaturutsira Akasidi akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babulo; ndipo mudzatenthetsa mudziwu ndi moto.

24. Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa.

25. Koma akamva akuru kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife comwe wanena kwa mfumu; osatibisira ici, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;

26. pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani ndifere komweko.

27. Ndipo akuru onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu.

28. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka dzuwa lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 38