Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 37:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakuturukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Aigupto ku dziko lao.

8. Ndipo Akasidi adzabweranso, nadzamenyana ndi mudzi uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.

9. Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Akasidi adzaticokera ndithu; pakuti sadzacoka.

10. Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Akasidi akumenyana, nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okha okha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wace ndi kutentha mudzi uwu ndi moto.

11. Ndipo panali pamene nkhondo ya Akasidi inacoka ku Yerusalemu cifukwa ca nkhondo ya Farao,

12. pamenepo Yeremiya anaturuka m'Yerusalemu kumuka ku dziko la Benjamini, kukalandira gawo lace kumeneko.

13. Pokhala iye m'cipinda ca Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lace Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Akasidi.

14. Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Akasidi; koma sanamvera iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akuru.

15. Ndipo akuru anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m'nyumba yandende m'nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende.

16. Atafika Yeremiya ku nyumba yadzenje, ku tizipinda tace nakhalako Yeremiya masiku ambiri;

17. pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwace, niti, Kodi alipo mau ocokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo, Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo.

18. Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndacimwira inu ciani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?

19. Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babulo sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?

20. Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere ku nyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 37