Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 36:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Makaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu.

14. Cifukwa cace akuru onse anatuma Yehudi mwana wa Nataniya, mwana wa Salamiya, mwana wa Kusa, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lace, nadza kwa iwo.

15. Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenge m'makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m'makutu ao.

16. Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzace, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.

17. Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?

18. Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pace anandichulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m'bukumo.

19. Ndipo akuru anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.

20. Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m'cipinda ca Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m'makutu a mfumu.

21. Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.

22. Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yacisanu mwezi wacisanu ndi cinai; ndipo munali moto m'nkhumbaliro pamaso pace.

23. Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'nkhumbaliromo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'nkhumbaliromo.

24. Ndipo sanaopa, sanang'ambe nsaru zao, kapena mfumu, kapena atumiki ace ali yense amene anamva mau onsewa.

25. Tsononso Elinatani ndi Deliya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 36