Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 36:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

2. Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israyeli, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse, kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.

3. Kapena nyumba ya Yuda idzamva coipa conse cimene nditi ndidzawacitire; kuti abwerere yense kuleka njira yace yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi cimo lao.

4. Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.

5. Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m'nyumba ya Yehova;

6. koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene aturuka m'midzi yao.

7. Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yace yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukuru.

8. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anacita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.

9. Ndipo panali caka cacisanu ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wacisanu ndi cinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ocokera m'midziya Yuda kudzaku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.

10. Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.

11. Pamene Mikaya mwana wa Hemariya, mwana wa Safani, anamva m'buku mau onse a Yehova,

12. anatsikira ku nyumba ya mfumu, nalowa m'cipinda ca mlembi; ndipo, taonani, akuru onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akuru onse.

13. Ndipo Makaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu.

14. Cifukwa cace akuru onse anatuma Yehudi mwana wa Nataniya, mwana wa Salamiya, mwana wa Kusa, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lace, nadza kwa iwo.

15. Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenge m'makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m'makutu ao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 36