Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 35:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pita ku nyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'cipinda cina, nuwapatse iwo vinyo amwe.

3. Ndipo ndinatenga Yaasaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habazinya, ndi abale ace, ndi ana amuna ace, ndi nyumba yonse ya Arekabu;

4. ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;

5. ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.

6. Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;

7. ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.

8. Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu amuna ndi akazi;

9. ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitiri nao munda wamphesa, kapena munda, kapena mbeu;

10. koma takhala m'mahema, ntimvera, nticita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu.

11. Koma panali, pamene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu cifukwa tiopa nkhondo ya Akasidi, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.

12. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 35