Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 34:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo akuru onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;

11. koma pambuyo pace anabwerera, nabweza akapolo ace amuna ndi akazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo amuna ndi akazi;

12. cifukwa cace mau a Yehova anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

13. Yehova Mulungu wa Israyeli atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, kuturuka m'nyumba ya ukapolo, kuti,

14. Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wace amene ali Mhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi cimodzi, mudzammasule akucokereni; koma makolo anu sanandimvera Ine, sanandichera Ine khutu,

15. Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kucita cimene ciri colungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzace; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene ichedwa dzina langa;

16. koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akacite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu amuna ndi akazi.

17. Cifukwa cace Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wace, ndi munthu yense kwa mnzace; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kucaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.

18. Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanacita mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwana wa ng'ombe ndi kupita pakati pa mbali zace;

19. akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwana wa ng'ombe;

20. ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za mlengalenga, ndi ca zirombo za pa dziko lapansi.

21. Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ace ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, imene yakucokerani.

22. Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo ku mudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 34