Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 34:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndi nkhondo yace yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wace, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yace yonse, akuti:

2. Yehova Mulungu wa Israyeli atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo adzautentha ndi moto;

3. ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lace, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lace; ndipo maso ako adzaanana nao a mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babulo.

4. Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;

5. udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! pakuti ndanena mau, ati Yehova.

6. Ndipo Yeremiya mneneri ananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda m'Yerusalemu,

7. pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babulo inamenyana ndi Yerualemu, ndi midzi yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti midzi ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.

8. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, atapangana Zedekiya pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;

9. kuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Mhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzace kapolo wace;

10. ndipo akuru onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;

11. koma pambuyo pace anabwerera, nabweza akapolo ace amuna ndi akazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo amuna ndi akazi;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 34