Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 32:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Cifukwa canji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo iye adzaulanda,

4. ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Akasidi, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;

5. ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babulo, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Akasidi, simudzapindula konse?

6. Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

7. Taonani, Hanameli mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.

8. Ndipo Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.

9. Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanameli mwana wa cibale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekele khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.

10. Ndipo ndinalemba cikalataco, ndicisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.

11. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wobvundukuka;

12. ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 32