Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 32:23-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndipo analowa, nakhalamo; koma sa namvera mau anu, sanayenda m'cilamulo canu; sanacita kanthu ka zonse zimene munawauza acite; cifukwa cace mwafikitsa pa iwo coipa conseci;

24. taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la, Akasidi olimbana nao, cifukwa ca lupanga, ndi cifukwa ca njala, ndi cifukwa ca caola; ndipo cimene munacinena caoneka; ndipo, taonani, muciona.

25. Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Akasidi.

26. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

27. Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu lonse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?

28. Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Akasidi, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzaulanda,

29. ndipo Akasidi, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa macitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu yina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.

30. Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Yuda anacita zoipa zokha zokha pamaso panga ciyambire ubwana wao, pakuti ana a Israyeli anandiputa Ine kokha kokha ndi nchito ya manja ao, ati Yehova.

31. Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiucotse pamaso panga;

32. cifukwa ca zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 32