Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 31:18-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Kumva ndamva Efraimu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwana wa ng'ombe wosazolowera gori; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.

19. Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ncafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, cifukwa ndinasenza citonzo ca ubwana wanga.

20. Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; cifukwa cace mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamcitiradi cifundo, ati Yehova.

21. Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israyeli, tatembenukiranso ku midzi yako iyi.

22. Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati; iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? pakuti Yehova walenga catsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.

23. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.

24. Ndipo Yuda ndi midzi yace yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

25. Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uli wonse wacisoni.

26. Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 31