16. Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti nchito yako idzalandira mphoto, ati Yehova; ndipo adzabweranso kucokera ku dziko la mdani.
17. Ndipo ciripo ciyembekezero ca citsirizo cako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.
18. Kumva ndamva Efraimu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwana wa ng'ombe wosazolowera gori; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.
19. Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ncafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, cifukwa ndinasenza citonzo ca ubwana wanga.
20. Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; cifukwa cace mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamcitiradi cifundo, ati Yehova.
21. Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israyeli, tatembenukiranso ku midzi yako iyi.
22. Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati; iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? pakuti Yehova walenga catsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.
23. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.