Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 3:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderana ndi nyumba ya Israyeli, ndipo adzaturuka pamodzi ku dziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.

19. Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, colowa cabwino ca makamu a mitundu ya anthu? ndipo ndinati mudzandicha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.

20. Ndithu monga mkazi acokera mwamuna wace monyenga, comweco mwacita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova.

21. Mau amveka pa mapiri oti se, kulira ndi kupempha kwa ana a Israyeli; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.

22. Bwerani, ana inu obwerera, ndidzaciritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.

23. Ndithu akhulupirira mwacabe cithandizo ca kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli cipulumutso ca Israyeli,

24. Ndipo cocititsa manyazi cinathetsa nchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao amuna ndi akazi.

25. Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutipfunde ife; pakuti tamcimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulunguwathu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 3