Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 3:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kucuruka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la cipangano ca Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzacitanso konse.

17. Pa nthawi yomweyo adzacha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.

18. Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderana ndi nyumba ya Israyeli, ndipo adzaturuka pamodzi ku dziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.

19. Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, colowa cabwino ca makamu a mitundu ya anthu? ndipo ndinati mudzandicha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 3