Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 27:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi caola, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babulo?

14. Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babulo; pakuti akunenerani zonama.

15. Pakuti sindinawatuma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupitikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

16. Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babulo posacedwa; pakuti akunenerani inu zonama.

17. Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babulo, ndipo mudzakhala ndi moyo; cifukwa canji mudzi uwu udzakhala bwinja?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 27