Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 26:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvera;

6. pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu citemberero ca kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

7. Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m'nyumba ya Yehova.

8. Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.

9. Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.

10. Ndipo pamene akuru a Yuda anamva zimenezi, anakwera kuturuka ku nyumba ya mfumu kunka ku nyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova.

11. Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akuru ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.

12. Pamenepo Yeremiya ananena kwa akuru onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mudzi uwu mau onse amene mwamva.

13. Cifukwa cace tsopano konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka coipa cimene ananenera inu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 26