Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 26:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Mika Mmorasi ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.

19. Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? kodi sanamuopa Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka coipa cimene ananenera iwo? Cotero tidzaicitira miyoyo yathu coipa cacikuru.

20. Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wace wa Semaya wa ku Kiriati Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau lonse a Yeremiya;

21. ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ace onse, ndi akuru onse, anamva mau ace, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Aigupto;

22. ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Aigupto, Elinatanu mwana wace wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Aigupto;

23. ndipo anamturutsa Uriya m'Aigupto, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wace m'manda a anthu acabe.

24. Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 26