Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, cifukwa ca lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.

28. Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga cikho pa dzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa.

29. Pakuti, taonani, ndiyamba kucita coipa pa mudzi umene uchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.

30. Cifukwa cace muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzachula mau ace mokhalamo mwace moyera; adzabangulitsira khola lace; adzapfuula, monga iwo akuponda mphesa, adzapfuulira onse okhala m'dziko lapansi.

31. Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.

32. Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.

33. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25